Article
Elon Musk wayambitsa chipani chake, ndipo zomwe wayankhula zadabwitsa anthu motele:

Elon Musk wayambitsa chipani chake, ndipo zomwe wayankhula zadabwitsa anthu motele:

Elon Musk wayambitsa chipani chake, ndipo zomwe wayankhula zikumveka za mangawa ndi a Trump.



A Elon Musk alengedza kuti ayambitsa chipani chawo cha American party koma pofotokoza cholinga cha chipani chi, zikuoneka akuzembelerabe president Trump kutengela kuyambana kwawo.

A Elon Musk alemba pa X kuti kuti ayambitsa chipani kuti anthu aku America apezenso ufulu chifukwa ulamuliro wa panopa wa a Trump sukuyendesedwa ngati democracy, ndipo anapitilila kunena kuti zimene akuchita president wapanoyu ndi zosaukitsa komanso zoononga.

A Elon Musk anaononga ndalama zochuluka kwambili ($288 Million) pothandizila campaign kuti Trump awine ndiye zikuoneka kuti zikuwapweteka kwambili mpaka aganiza zongoyamba chipani chawo.

Koma fuso lagona pokuti Kodi zizatheka kuti a Elon Musk aimile ngati president? Kutengela kuti iwowa sanabadwile mu dziko la America ndipo sizikudziwika ngati chipani chi chaka lembetsedwa kale ku US election authority kapena ndi chipani cha pa social media basi.

Mukuona kuti a Elon Musk apanga chiganizo chabwino kuyambitsa chipani chawo

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!