Article
Waulura ekha Chinsisi Chomwe anapanga kuti amange nyumba yotereyi

Waulura ekha Chinsisi Chomwe anapanga kuti amange nyumba yotereyi

Student wina wamkazi wa ku South Africa wamanga Nyumba Pogwiritsa Ntchito Allowance Komanso ma servings ake a Ku University komwe akuphunzira

Pa nthawi yomwe ophunzira ambiri amadandaula za kusowa kwa ndalama kapena amakalipidwa chifukwa chogwiritsa ntchito ndalama mosasamala, nkhani ya tsikana uyu yaimira ngati chitsanzo chapadera cha kuganiza patali.

Tikunena pano anthu ambiri pa social media Omwe amva za nkhani ya tsikana uyu adabwisika ndipo alimbikisika komanso ena akufunsa njira zomwe anagwiritsa ntchito posunga ndalama zokwana mpaka kumangira Nyumba yi zinatheka bwanji?

Kodi ndalama zonse zomangira nyumbayi zidalipiridwa ndi allowance yokha ndi ma servings basi? Kumanga nyumba kwa mtsikanayu kwayambitsa zokambirana Ndipo anthu ambiri akufunsana

Asanafotokoze chinsisi chake chomwe anapanga kuti plan yake yomanga nyumba ndi ndalama ya allowance komanso yomwe amasunga iye anaponya video pa TikTok akuwonetsa magawo osiyanasiyana a ntchito yomanga — kuyambira pomwe anayambira foundation yomanga nyumbayi mpaka makoma akukwera pang'onopang'ono. M’mawu omwe walemba pa video, mtsikanayu anasonyeza kuti wagwiritsa ntchito ndalama zake za ku sukulu popanga polojekiti imeneyi

Komabe anthu ena ansanje anayambapo kuyankhura zambirimbiri Ndipo iye sanakwiye m’malo mwake anayambapo kuwafotokozera m’mene wakwanisira kumanga nyumba yakeyi ndi ndalama yosungira, Ndipo tsikanayu anayamba ndikuyankhura kuti

“Inetu ndakhala ndikukhumbira nditakhala ndi nyumba yanga kuyambira kale kale kotere ma plan anga omanga nyumba sanayambe lero ndimati ndikapeza let’s say 100K ndimachotsapo 30% ndikusunga, choncho mpaka ndinakwanitsa kupeza ndalama yoyambira kumanga project imeneyi and izi ndinaziyamba in my first year and now ndili 5th year mpamene ndikumalizisa”

Nkhani ya tsikanayu ngakhale wafotokoza mene anakwanitsira kusungira ndalama Komabe ena sakukhulupilira Ndipo yausa zokambirana zazikulu mdziko lonse zokhudza kudziwa kugwiritsa ntchito ndalama bwino, kusunga, komanso momwe angapangire bwino m'tsogolo ndi mwayi waung’ono omwe aliyense atha kukhala nawo.

Kodi inu maganizo anu ndiotani pa nkhaniyi? Izizi ndizothekadi kapena mukuganiza kuti anagwiritsa ntchito njira Zina?

Admin Jeffrey

Comment Below

5 Comments

Charles

Eya nagwirisadi tchito ndalama yosunga 100%

Charles

Eya nagwirisadi tchito ndalama yosunga 100%

Jonathan chiumia

She is a wise woman n genius

Joe

Ndizotheka ndipo 100% vuto k1000 kumalawi timaitenga yochepa kuti sungamange nyumba tangoyesela kusunga 1k or 2k pa tsiku pokutha pa chaka chimozi sungagule malo?izizi mzotheka amwene

Gift

Ndi zotheka kumanga nyumba ndi ndalama zomwe akunenazo....kmaso sukulu yake si ku malawi

upload your music with us to get maximum reach out!