Ndichifukwa chani Dziko la Iran ndi Dziko la Israel likumenyana potumizilana mabomba omwe akupha anthu?
Kwa masiku angapo tsopano takhala tikuona pa masamba amchenzo kuti Dziko la Iran ndi Israel akumenyana Koma nkutheka sitikumvetsesa kuti kodi akumenyana chifukwa chani
Kotero mukamamaliza kuwerenga nkhani iyi mukhala mutadziwa kuti maiko awiriwa anayambana chani? Akumenyana chifukwa chani? Ndipo padakalipano amene akuiwina nkhondoyi ndi ndani?
Iran ndi Israel ndi mayiko awiri amene akhala akukangana pomenyana kwanthawi yayitali. Kumeneku kumachitika chifukwa cha zifukwa zosiyanasiyana, makamaka zandale, chipembedzo, ndi zikhulupiliro za madera ena.
Israel ndi dziko la Ayuda (Aisraeli), ndipo ambiri mwa Ayuda amakhulupirira Chiyuda. Iran, kumbali ina, ndi dziko la Achi Islam a mtundu wa Shia. Mayiko awiriwa samagwirizana pa mfundo zambiri, ndipo aliyense amaona winayo ngati mdani wake
Chimodzi mwa zifukwa zazikulu akuti Iran imathandiza magulu a nkhondo ngati Hezbollah ku Lebanon ndi Hamas ku Gaza – magulu amene amalimbana ndi Israel.
Israel, nawo, amaona kuti Iran ikufuna kuwononga dziko lawo, chifukwa Iran imanena kawirikawiri kuti Israel simayenera kukhalapo
Chiopsyezo china kwa Israel ndichoti akuti Iran ikupanga zida za nyukiliya, ndipo Israel imati izi ndi chiopsezo chachikulu. Choncho, nthawi zina Israel imachita za nkhondo ngati kuwomberapo malo a Iran kapena anzawo, ndipo Iran imabwezera.
Mikanganoyi si yatsopano, ndipo anthu ambiri akufuna mayikowa asamamenyane nkhondo, koma apeze mtendere. Koma mpaka pano, mikangano ikupitilira.
Nanga dzulo kwachitika Chani?
Pamene nkhondo ili mkati pakati pa Iran ndi Israel izi ndizomwe zachitika dzulo madzulo
Iran inatumiza mabomba ku Israel Ndipo yapha asilikali otsogolera Nkhondo Ndipo nayo israel inabwenza mabomba ku iran mokuti anthu ambiri avulala zinthu sizilibwino Komatu ngakhale zili choncho dziko la iran ladziwa kuti dziko la israel likuthandizidwa ndi dziko la United States of America
Izi ndi mwa zina zimene zachitika dzulo komatu nkhondoyi monga tanenela kumayambiliro muja si nkhondo ya lero anthuwa anayamba kumenyana kale kale ngakhale mu bible muli nkhani zawo zoti ankamenyana Koma funso mkumati kodi sangangokhululukirana ndikukambirana? Chikuvuta ndi chani?
Kma zovuta eeeeee akupwetekana
Mbolatu izi
Eee😂😂
Eee zosakoma
Bola kuno,timagona tavula zonse zovala
Iran iphan ana onse a Israel komaso America
Mmmm akambirane koma cz khondo siyanwino
Keep on updating 🔥
Keep on updating 🔥
Mesa ndi zolembedwa kale bayibulo kuti amathibulana kodi
WW3
This war sikutha coz of bias report like yanuyo, Israel started striking Iran koma apa munena ngt its Iran who started... Learn to be neutral first don't be like BBC And other propaganda medias
Ikathera kuwaya
Amenyane bas Asiye kudelelana Amadelelana kwambili Ndale involved iii singathe anytime soon Kufa kulipo azibale athuwo eshhh😭😭😭
World War 3 is loading chifukwa all parties are supported by other powerful countries
Ngakhale anthu angayesetse kupanga ngwirizano pofuna kukhazikitsa mtendere izi sizingatheke. Amayambaso ndi azitsogoleriwo kuphwanya malamulo angwirizanowo. Mmalo mokhazikitsa mtendere, mpamene mkangano umakulirabe
Asiyeni agobane
This people can never stop fighting coz all zipembezo zawo nde zmakamba zosiyana sure
Zikungokhala ngt movie tu 🤣
3 years ago before the fight of war between Israel and Gaza my friend told me that when these two nations fight against each other the world war will start again, so i think he right kkkkkkkkkkkk
Koma zikuchitikazi mmm
Za in-sha-allah
Za in-sha-allah
Palibe chiopyezo choti nkhondoyi itha kupitilira mpaka kuzatikhuza ife?
Izi nde zaonjeza
Lord ha e Mercy
Akakhala Jaki watiuza Kale Kutii.. Israel inaponya mabomba awo ku Iran Popanda Chifukwa so Iran ikubwezera..inuyo I think Nkhaniyi Mufotokoza moona mbali
It's not there is
Chifukwa chot a Israel Ali nd Mantha oti atha kulandidwa ma industries
Uli bhoo
Amene aiyambitsa ndu a Israel iran yachita kubweza dzulo
Afuna kuyambitsa third world war
So sad zamasik omaliza idzi
Only God Knows
zovuta bwanji
Kodi simungatipemphereko ka nkhondo ka friendly ndi israel ku bomako 😋 angotichangamusako wezi
Eeee zinthu Zake zosakhala bwno ngati zinatamba pakathawi nde kt sizingathe pano
Aslamu ngamakani ngat amadziwa nkhondo awachape
Ayi zikomo
zochitika m'masiku otsiriza
Akwapulane basi hiyaaaa
Kodi anthunu baibulo mumaliona ngati chani?
Nanga Chifukwa chiyani USA ikulowelela nkhondo imeneyo??
Abale inu muzatiphesa😥
Iran 🇮🇷 osamaishosha dala ndi akulu akulu aja
Tiyeni tiwalore akwapurane basi ife we are not afraid of loosing anything simply because we don't have nothing
So sad 😥😥😥
Aphane
Ndi zolembedwe malemba adzakwanilitsidwe
So sad 😢😭💔
Zosakhala bwino
Mmmm nde zovutatu
Nkhondo iyi singathe, ndipo sizatha. Tinayipeza ndipo tidzayisiya.
Kwamene amawerenga bible izizi sizachilendo
BA easy zith
Ngat nkhondoyo m bible ilimo ndye Kut singathei mophweka.
Zovutatu apa.
Chiyambi cha third world war ichi
Zingofunika world war 111 iyambike basi
Zonenedwa mu Bible simungachiletse ndi ulosi basi
zinthu zina zimangoyenela kuti zichitike,zinthu monga nkhondo ndi zina mwa izo,ndi chifunilo cha Allah,tiyeni tipemphe mulungu wachifundo atifewesere moyo wachipembezo kuti tizapulumuke, Mulungu wamphamvu yomse ayang'anile ndikutchinjiliza anthu aku Gaza kmanso Israel kmanso mayiko ena omwe alipa nkondo,Ameen
Ngati America yo ikuthandizadi Ndiye Iran iponyeko mabomba angapo ku united state ko
Zoonadi zomwe amafuna anzathu wa nzosagwila chipembezo Chika khale chimoz kut chani aziswana chomcho
Imeneo mwiña ena simumadziwa mpakana pano kuti mikangano simatha bwanji The answer is Israel akuimira Mulungu pomwe Iran akuimira Satana so mufufuze zipembedzo zawo anthu you'll agree with me kut ndinkhondo yapakati pa Mulungu ndi Satana yomwe imachitika pamenepa and even ma Israel eniakewo samavetsa kupatula okhawo omwe alindi choonadi mmitima mwawo
Nkhani iyiyi siyngathe mpaka pazafike poti American nayo yayamba kumenyanako ga ground osati zobisalira kumbuyo jwa Israeli
Dziko lapasi silingakhale bata pokha pokha Mulungu adzaweru izi ndi ziwanda za pweya wa nkhondo tiyen tizipephera tikapeza nthawi mtendere ujah umabweretsa chimwemwe zikomo kwambir tadziwa nawo zina apa makosana ntchito mukuyigwira potorera Data za m'mayiko ena......
Eish,, zosakhala bwino
World War 3
Very sad
Tizafa....
Sizingatheke chifukwa a Islam amafuna chipembedzo chikhale chimozi dziko lose zomwe Israel singalole
Eeeeish this will to an end of world
Zovuta kwambiri
Akanangokambiran bac izi sizabwino🙇😩
Eshi zovuta
Eeeeeh akhululukirane km
Thanks for your updating
Kuyambanso kwa world 🌎 war season 3💔
Nkhani zovuta kwabs
Thank you for sharing.