Article
Boma likufuna kuletsa Kukhalisa pa social media, pa zifukwa izi:

Boma likufuna kuletsa Kukhalisa pa social media, pa zifukwa izi:

Ana sakuyenela kukhala pa social media mpaka 2 hrs" afotokoza motelo pa chiganizo chofuna kupanga control kagwilitsidwe ntchito ka internet ndi social media;

Pamene mayiko ambili aku Africa sitikhala busy kwenikweni kupanga control kagwilitsidwe ka internet, kafukufuku waonetsa kuti internet komanso social media ambili akuigwilitsa ntchito molakwika.

Mmalo moigwilitsa ntchito ngati Malo opezelapo uthenga ophunzitsa komanso kugwilitsa ntchito zotukula miyoyo, ambili zaonesa akugwilitsa ntchito internet pa zinthu zongosewela ndipo zaonesa kuti anthu ambili asintha chikhalidwe pokopela kwambili moyo wa ena pa internet.

Pa chifukwa ichi akuti ambili akumakhala ndi nkhawa pakuti akumaona kuti akusalira, komanso ana zikumawaononga kaganizidwe. Kotelo boma la UK lapanga propose kuti pakhale limit pa kagwilitsidwe ntchito ka social media.

Kotelo akuti munthu akuyenela azigwilitsa ntchito social media ya yi kwa 2hrs yokha, kuti kwinako azikakhala busy ndi ntchito zake, kupeleka nthawi kwa banja lake komanso anzake. Iwo anati kubwela kwa ma social kukusokoneza anthu chidwi pa ntchito komanso pa ma banja awo.

Kotelo lamulo li koyamba liyamba kaye kwa ana, kuti asamagone mochedwa komanso kukomedwa kwambili ndi internet, ndekuti 2hrs ikatha basi ma account onse azizitseka okha.

Izi eni ma social media sanagwilizane nazo akuti aliyense ali ndi ufulu, pakuti akudziwa business yawo itsika izi zikachitika. Inu mukuona kuti ndiza nzeru kupanga zotele?

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!