Mzimayi yemwe pakadali pano ndi yekhayo wa mtali pa dziko lonse ku azimayi, anauzidwa kuti alipile mipando ya anthu 6 kuti akwane mu ndege pa ulendo wake.
Mzimayi yu amene ali otalika 7ft 0.7 inches, anakakamizidwa kulipila mipando ya ndege yokwana 6 kuti iyeyo akwane kutengela ndi kutalika kwake. Izi zili chomwe chi pakuti iyeyu sizingatheke kuti akhale pansi ndekuti azigunda denga, kotelo amayenela kukhala chogona kuti akwane bwino.
Mzimayi yu yemwe dzina lake ndi 'Rumeysa Gelgi', ali mu mbili ya Guinness World Record ngati munthu wa mtali kwambili yemwe amavutika kuyenda pa ndege, pa galimoto kapena sitima chifukwa samakwana kukhala pansi.
Iyeyu akuti wakhala akungokhala kunyumba ndiye potengela kuti wakwanitsa zaka 28 anafuna kuti ayambe po kuzungulira dziko la pansi, kotelo anadabwa akumuuza kuti agule ma ticket a anthu 6 kuti akwane, koma zikuoneka kuti anali okonzeka kutelo chifukwa zinatheka di.
Tikunena pano iyeyu akuti wangoyambapo, ndipo akhala akuzungulilabe mayiko ambili, ngakhale kuti amamukweza pachi thandala ngati odwala kuti ayende bwino.
Mzimayi yu kwawo ndi ku Turkey ndipo iyeyu anapezeka watalika chonchi kutengela condition yomwe alinayo ya weaver syndrome yomwe zosatila zake munthu amangotalika, moti olo kuti ayende amadalira wheelchair.
Moti wapempha anthu omwe amapanga ndege komanso ma galimoto kuti asamapange zinthu zongokwana antu afupi afupi, iyeyo so amuganizile.
Nde mwati amuganizile kumpangila yake ndege 🤣🤣🤣🤣🤣
Ok comment received
Aaah zoona