Kutengela chiwembu chomwe chachitika, Pali chiopyezo cha nkhondo ya dziko lonse kutengela zomwe Ukraine yapanga ku Russia relo.
Dziko la Ukraine lapanga chiwembu Chachikulu ku Russia, zimene ambili sanayembekedzele kutengela kuchepa mphavu kwa dziko la Ukraine. Chiwembu chadodometsa dziko la Russia ndipo mayiko ena ayamba kuopa kuti ngati Russia ingabwenze chiwembu chi pogwilitsa ntchito mabomba a Nuclear. Zipangitsa mayiko ena kulowelerapo zomwe zingayambitse nkhondo ina yaikulu kwambili.
Nkhani zonse zi zachitika, kusatila pamene Donald Trump anayankhulana komanso kupempha President waku Russia a Putin, kuti athese nkhondo imene ilipo ndi Ukraine. A Putin analorela kupanga mkumano okambilana ndi president waku Ukraine kuti apange zothesa nkhondo yi. Koma tsiku la mkumano litafika a Putin sanapite nawo ku M'kumanowu.
M'malo mwake tatangotha masiku awili a Putin anapezeka atumizanso mabomba kukaphulitsa ku Ukraine posatengela kuti panali maganizo ofuna kuthesa nkhondo yi. Izi zinakwiiyisa mayiko ambili aku Europe kuphatikiza po a Trump, mpaka President waku America yu anasinthana mawu ndi akulu akulu achitetezo komanso a ndale aku Russia ndikumaopyezana.
Prime minister waku Britain 'Keir Starmer' wayankhulapo kale kuti, pazimene zachitikazi chilichonse chitha kuchitika kotelo dziko lawo panopa lingoyenela kukhala lokonzeka chifukwa ngati Russia itasankhe kupanga chiwembu Chachikulu Britain izayeneleka kupanga po kanthu kuteteza Ukraine.
Tikunena pano mayiko ambili aku Europe ali mbali ya Ukraine poganiza kuti dziko la Russia ndi lomwe likulakwitsa. Pamene dziko la Russia lilonse ndi abale ena ngati China komanso North Korea omwe anthu a kuganizila kuti atha kuteteza a Russia ngati ali mmavuto.
Munsimu muli video imene ikuonesa dziko la Ukraine ikuphulisa malo amene Russia imasungila ndege ndi zida zina za nkhondo, ndipo ma report akuti chiwembu chi chaononga ndalama za nkhani nkhani
Watch: https://vm.tiktok.com/ZMShxGofE/