Article
Zomvetsa chisoni Zomwe wayankhura Bambo atasisimuka pamene anakomoka

Zomvetsa chisoni Zomwe wayankhura Bambo atasisimuka pamene anakomoka

Agwa pansi ndikukomoka atamva kuti Mkazi wake wabereka ana 5

Bambo wina dzina lake Adamu Muhammed adagwa pansi atamva kuti mkazi wake wabereka ana 5 pakamodzi

Malingana ndi anthu omwe anali pamalowa nthawi yomwe bamboyu amauzidwa uthenga wabwino kuti mkazi wake wabereka ana 5 bamboyu adagwa ndipo ogwira ntchito m’chipatalachi adathamangira kumuthandiza ndipo adakwanitsa kumudzutsa

Bamboyu atasisimuka anayankhura motere
“Zikomo Mulungu chifukwa cha Mphatso ya ana yomwe mwandipatsa koma ndikulephera kumvetsa.

Sindinadziwe kuti tikuyembekezera mapasa 5 Tsopano, tilibe chuma kapena ndalama zokwanira kulipira m’chipatala, komanso kusamalira ana atatu nthawi imodzi” bamboyu anatero uku misodzi ikutuluka

Iye anafotokozaso kuti iyeyu budget yokonzekera inali ya mwana modzi osati mpaka 5 pakamodzi ayi

Anthu omwe anali pomwepo adatsimikizira kuti kubadwa kwa ana kunayenda bwino, koma banjalo likufunika thandizo la mankhwala, zakudya, ndi ndalama posachedwa kuti lisamalire ana.

“Banja limeneli likufunika thandizo mokuti Tikupempha boma ma NGO, magulu achipembedzo, ndi anthu ena okoma mtima kuti athandize” akubanja anatero


Nkhaniyi yachitika ku Nigeria Muli inu mungatani?

Admin Jeffrey

Comment Below

17 Comments

Luke williams

Ndingapangeso bwanj koposa kuthokoza?mulungu sangasokoneze olo pang'ono

Precious Matako

God's plan always sungavetse

Viecon

Kufela2

Lukia kasim

China chilichonse chimene mulungu a atipatsa amakhala Ali ndi cholinga komaso mulungu amatiyesa pofuna kutiona ku khulupilila kwathu mulungu amakhala ndi cholinga pa chilichonse

Yusuf Banda Brown

God bless you

Kacmu

Muzomse yamikani yehova, Ali ndi cholinga powapasa ana omsewo,

funique

Pena mablessing akachuluka zimatheka kufainta ndithu

Noic

Mmmmm mkanachita zomwezo coz sizimene ndimaembekezera

Joel Mumba Anthony

It's a blessing from God, let's accept the situation no matter how, but God's name cannot be ashamed, He already made ways on how the family and the new comers will live and survive, we specially thank God for the protection to the mother, because since she conceived, eeish she has been in a tough condition, and giving birth to 5 at once and then all are alive it's not easy, praise God, I pray that the family should lack nothing

Shadreck

Chimudalitso Cha mulungu osazachiphweketsa 🎉😍🙌🙏

Ayesha Jack

Zabwino kwabasi

Spu

Blessed family

Luka Thamanga

Mphaso iyi yaposera maganizo athu mene timaganizira

Samson Uladi

Akamati chimdalitso mchimenechitu kkkkkk azabeleke chocho achina uje ulemera aja akhoza kusangalalatu

Ruth D.Chawinga

Kungoyamika kumwamba basi zonse kumusiyira Ambuye osadandaulaso zamavuto.Adabwa mkomwe kuchokere thandizo anthu aliko achikondi

Kkkkkkkkkkk

Kkkkkk

RAFIQUE

Ok

upload your music with us to get maximum reach out!