Article
Mkulu amene anayambisa KFC yake amumanga, pa mulandu opusisa ogula

Mkulu amene anayambisa KFC yake amumanga, pa mulandu opusisa ogula

Anayambisa KFC yake ndipo a Police atadziwa amumanga, pa mulandu opusisa ogula.

Mkuluyu yemwe ndi waku South Africa, wamangidwa atapezeka kuti anatsegula KFC nyumba mwake, ndipo amatenga ma order ngati mmene imachitika KFC ndikumapanga deliver.

Izi zachitika kwaka nthawi ndipo ogula anayamba kuchulukila ati pakuti KFC yakeyi imapanga zokudya zokoma kuposa ma KFC eni eni wo. Ndiye alipo waiphedula amene samamuonela kukodwa mkulu yu.

Ndiye tikunena pano kuli mkangano ena akuti a police ali ndi nsanje chabe, pamene ena akuti ayi amuchita bwino amapangawo ndi mulandu. Iyeyo sangamazitchule KFC zili zaboza. Inu mbali yanu Mukuona kuti zalakwika kapena ayi?

Pamene a Malawi amene ali ku South Africa angoyankhulapo kuti, zoona Lulu sananame kuti kumawasamala ma neba. Nanga business ya bwino bwino munthu amadalira, koma ma neba angomupachika mpaka kumumanga. Zosayenda

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!