Kwa onse osata fashion, chibangili ichi chikugulutsidwa 8.6 Million. Inu mungagule?
Chibangili chi achipanga ndi a Balenciaga ndipo chikumaoneka ngati celltape, chabe kuti mkati mo mukumaoneka mawu olemba Balenciaga.
Ndiye pakuti ku Malawi kuno nkhani za fashion ndiye timazitengela, bracelet imeneyi ikugulitsidwa $5,000 yomwe ku Malawi ili 8.6 Million.
Chinthu chimene chi chapangidwa ku France ndipo amene apanga wo akuti akufuna tsopano fashion ilowe ku zinthu zomwe timazigwilitsa ntchito kale. Ndiye akumemeza onse osata Fashion kuti agule. Akuti osamangozimva uyoo, mayoo eni eni ayamba kudziwilana bracelet yowoneka ngati Cell tape yomatila ndalama yi.
Azungu ena anena kale kuti iyi ndi fashion yopusa ndipo mwina akayese ndi anthu aku Africa omwe wo koma iwo sakupanga nawo. Ndiye Malawi mbali yanu mukuti po bwanji? Press your order
Aaaaaa zopanda phindu
AAAAH CHACHANI?