Bambo wina wa ku Uganda emwe ali ndi ana okwana 102 ndi zidzukulu 568 basi waganiza kuti asiile pompo kubeleka
A Musa omwe ali ndi zaka zakubadwa zokwana 70 tsopano awuza akazi awo onse 12 kuti ndi nthawi yoti apume ndikubereka ana atsopano ngakhale kuti nyonga zawo sikuti zathera pa ana 102 po ayi Koma pazifukwa zomwe iwowo azifotokoza Kulibwino asiile kaye pompo kufikira zifukwazo atazikonza atha kumazapitiliza kutsogoloku
Tisanakambe zifukwa zomwe a Musa awuzira azikazi awo kuti aime kaye kubereka tikambeko history Pangโono ya a Mussa
Iwowa akuti dzina lawo lakubadwa ndi Mussa Hasahya Kasera ochokera ku Uganda, Butaleja District Ndipo khumbo lawo lakhala lozakwanilisa Malemba a Bible โBelekanani ngati Mchengaโ Ndipo zonsezi zinayambira Ndi Mkazi wawo oyamba amene anaberekelana naye ana okwana 15 Koma ataona kuti mphamvu zawo zikuchulukabe anakwatiraso wina kenakoso wina, kenakoso wina Mpaka kukwana Akazi 12
Tsopano nkhani yaikulu apa ndiyoti ndichifukwa chani a Mussa aganiza kuti achite break khwee! kukhalabe ndi ana ena anyuwani kuonjezera pa 102 omwe ali nawo kale?
Malingana ndi a Musa iwo afotokoza kuti kale kale anali ndizochita zogwirika Ndipo zimawayendera amakwanitsa kudyesa mabanja onse 12 koma pano chifukwa cha kukwera kwa zinthu komanso kusowa kwa ntchito Komanso ma business awo anasiya kuyenda ngati kale Ndichifukwa aganiza kuti ayambe ayima kubereka ana kuti kangachepe komwe ali nako akwanitsebe kusamalira ana 102 ndi zidzukulu 578 zomwe padakali pano ali nazo
A Musa anenesa kuti iwo nyonga adakali nazobe Koma mavuto a kusowa kwa ndalama ndiomwe awabwenza mbuyo kuti apange chiganizo choti awuze akazi awo onse 12 kuti ayambe ayima kaye kubereka ana atsopano
Greet madala
Aaaa aonetsa zisuzo
Madala aiwonela kutali sakwanisa kudyesa
Adawa amasatirad bible
Eewee komatu ntchito aigwira abambo awa ichiiii
Ofunika makosana muvaye mukangowapanga sapot system ๐
Munthu ND yemwey mussah
Owoo? Zina ukamva
Mbaka ana 102
Solomoniology
Nzovuta kwambiri and sindikuvesabe ...mpaka akazi 12 ayi Zikomo
Anthu kunjakutu akupakula beansness osati zibwana๐๐๐
Despite kukwanilitsa malemba komano pa zaka zawo iwowo akufunika angosiya basi nanga azichita kupikisana ndi ana awo kubeleka
Nde akundiuza kut anawo samagwira ntchito kuzithandiza okha coz akuoneka ndakulutu mpaka zizukulu
Ndalama alinazo.opanda kanthu sangakwanitse zimenezi
Mphanvu bas
Kkkkk Koma voto anawo sangapuzile
Eeee koma yaaa ndee Ali ndi mphamvu
Money talks .
Koma yah ๐๐๐, mukufuna kukwanirisa malemba et
Economy yake imene mpaka 102, ana amenewo palibe angaphunzile school
A Mussa kod ndnu sheikh??
Apa nde malembo awakwanitsadi chifukwa 102 +578 eeeeeh ndi mzindatu
Ulemu wawo a musa uku nde kukwanilitsa malemba
Mmmm koma ndiye mpaka 102 eee ameneyi amafunadi kukwanilitsa malemba
Koma ndiye , enafe ana awiri akulephera kudyetsa
Awa ndi makina opangira katundu wa boma
Koma ndie mulutu
Ana 102 ๐๐๐๐๐๐angakhale ndimudzitu uyu