Kutengela chithunzi chomwe chinagawidwa pa social media ndi wamkulu wa kale wa FBI "Pali Chiopyezo chokuti a Trump atha kuphedwa" a chitetezo atelo chifukwa:
Kwatuluka chithunzi chimene odziwa za chitetezo atanthauzila kuti, zomwe zalembedwa pa chithunzi cho ndi mawu oopyeza kuti president waku America a Donald Trump alipo akufuna ku wachita chiwembu ndikuwapha. (Death Threat)
Izi zachokela pamene munthu wina yemwe anali wa mkulu wa FBI Mr James Comey anaika pa social chithunzi chomwe chinalembedwa kuti '8647'. Tsopano kwa nthambibyoona za chitetezo Inatanthauzila kuti chithunzi chi chili ndi uthenga wakuya ndipo akufotokoza za chiwembu chomwe chi kufuna kuwachitilila a Trump.
Otanthauzila wo ananena kuti nambala ya '8647' ikutanthauza zotele, 47 wa kumapeto yo akutanthauza a Trump amene ali President wachi number 47 ku America ko. Pamene 86 kutengela dictionary ya 1930 nambala yi imatathauza kukana chinthu kapena kuti kupha munthu kumene.
Kotelo nambala yi kupangidwa share pa samba la mchezo ndi munthu okuti anali wa FBI komanso akukhulupilira kuti ali ndi udani ndi a Trump, uthenga wu sunatengedwe mopweka mpaka mwana wake wa Trump anapita kukalemba pa tsamba lake la mchezo modandaula kuti "wa mkulu wa FBI wakalekaleyu Mr James Comey akufuna kupha bambo ake chifukwa chani?"
Ndipo director wa Homeland security, anasimikiza za nkhani yi ndipo walengeza kuti kafukufuku wayambika pa nkhani yi pakuti nawonso akukhulupilira kuti chinthu zi chi ndi death threat ndithu kwa a Trump.
Koma a Comey ayankhulapo kuti Iwowa ma nambala wa anangowapeza atalembedwa mphepete mwa nyanja pa mchenga, sanadziwe kuti ena atanthauzila izi mu njila imeneyo. Zomwe zikutanthauza kuti iwowa sanaike chithunzi chi pa zolinga zimene anthu wa atanthauzila chithunzi chi.