Article
Kodi Kuyankhura Kutereko cholinga Burna Boy zimupweteke?

Kodi Kuyankhura Kutereko cholinga Burna Boy zimupweteke?

Uku ndiye kufuna Kupalana mkamwa ndithu Ndipo uwu ndi Mtopora waukulu

Ex wake wa Burna Boy Stefflon Don akupitilizabe kugeya mwano mwankachibisira kwa Burna Boy,

Pamene Burna boy walengeza kuti akufuna apereke ndalama kwa President wa ku Burkina Faso Ibrahim Traore pantchito yabwino yomwe akupanga ku dziko lake komanso kupereka example kwa ma president muno mu Africa ndipamene Stefflon Don naye wayankhura pa social media pake kachikenaso kuikilapo ndemanga amvekere

“Ibrahim Traore is the real African Giant I repeat”

Izi zakwiisa ma fans a Burna Boy amene akuti ichi ndichipongwe kwa Burna Boy chifukwa akamati African Giant ndi Burna Boy ekha basi ndiye chifukwa choti Traore akupanga zinthu ZODABWISA kapena kuti zosangalasa mu dziko lake sizikutanthuza kuti walanda u African Giant

Last month Stefflon Don Ex wake wa Burna Boy emweyu analembaso pa social media amvekere “ Ibrahim Traore is incredible, In my next life, want to marry him”

Pamene tikunena pano ma fans a Burna Boy Ndipo ma fans a Burna Boy ndi Traore ayambapo kumuthira Fire Oimba wa ku London Stefflon Don kuti chonde asawadanise anthu by comparing them

Admin Jeffrey

Comment Below

10 Comments

Brian Mtambalika

Eeh kwachematu

Clif Maseya

Ziliko

Clif Maseya

Ziliko

Foster

Zachabe

Alkel thinol

Tili pheee kuma stand kuwonelera

Kasisi Carpenter

Seen it

sofarbigyao170@gmail.com

Koma Che jefule mwe

Jhanga Bosco

Wausilu ameneyu sure

Medson

Noted but Burna Boi is my African Giant forever

Martin namakhwa

It's just incredible issue anyway its life

upload your music with us to get maximum reach out!