Article
Munthu amene wayikidwa ziwalo za Nkhumba, wapulumuka ndipo zakhala chonchi;

Munthu amene wayikidwa ziwalo za Nkhumba, wapulumuka ndipo zakhala chonchi;

"Ziwalo za Nkhumba zitha kumagwilisidwa mu nthupi la munthu" atelo a Chipatala pazifukwa

Kutengela kuti anthu amene ali ndi mavuto a ziwalo ngati kidney, mtima komanso mapapu akuchulukila. Mbuyo monsemu anthu akhala akudalira anthu anzawo kuti azipeleke ziwalo zomwe zimakhala zovuta kwambili ndipo nthawi zambili anthu amavutowa amangopezeka amwalira.

Tsopano a Chipatala apeza kuti tsopano ziwalo za Nkhumba zitha kuthandidzila kukonza vuto li. Iwo anena so kuti nkhumba ndi yabwino kutengamo chiwalo kuika mwa munthu pa chifukwa chokuti matenda amene imagwila nkhumba samatheka kupasilana ndi munthu. Izi zanenedwa kupangila mbuyomo a science ena anayesa kumatenga ziwalo za a nyani akulu akulu ndi kuika mwa munthu. Izi zimapezeka munthu ali ndi matenda ena odabwitsa omwe wapasilidwa ndi anyaniwo.

Iwowa apitiliza kufotokoza kuti nkhumba ubwino wake imakhala yaikulu ku mathamangila Kukula kwa mimba ya munthu. Kotelo mapapu, ma kidney komanso mtima wa nkhumba size yake ndi wa munthu sizosiyana kweni kweni. Kotelo nkhumba ndi njila yokha yo yothandi kusowa kwa ziwalo ndipo akuitchula kuti Xenotransplatation.

Tikunena pano anthu ena ayambapo kale kulandila thandizo li, ndipo akulu ena otchedwa Tim Andrews aikidwa kidney ya nkhumba yi. Izi zawathandiza pamene ankapasidwa masiku amene angakhale ndi moyo ngati salandila chithandizochi, ndipo mbuyo monsemu amadalira ma machine kuti apeze bwino.

Ndipo relo wasanduka hero, akuti anali ndi chikayiko ndithu, koma anangokhulupilira kuti ichi chimene akuyenela kupanga kuti ayese kuzipulumusa ku matenda wa.

Inu mungalole kuikidwa ziwalo za Nkhumba?

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!