Article
Anthu a Science akuti apeza kuti dziko litha pompano, ndipo atchula dzaka zomwe zasala

Anthu a Science akuti apeza kuti dziko litha pompano, ndipo atchula dzaka zomwe zasala

Mpungwe pugwe wayamba pamene gulu la anthu a Science akuti apeza kuti dziko litha pompano, ndipo atchula dzaka zomwe zasala.

Iwowa akuti kutengela kafukufuku wawo amene amathandizidwa ndi ma Computer, apeza kuti dziko likuonongeka komanso kuola mwachangu kuposa mmene amaganizila. Ndiye akuti kwasala nyenyezi zizangosowa Kenako dziko lonse m'dima.

Pakafuku fuku amene anapanga mbuyo mo iwowa analosela kuti ndi mmene chilengedwe chikuyendela, dziko likhoza kumazatha pakatha zaka izi (25,937,424,601,000,000,000,000,000,000,000 years)

Komano kafukufuku wapangidwa panopa akuti apeza kuti dzaka zatsika kufika pa (10 quattuordecillion years)
Yomwe ili (10,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000,000 years)

Mwachidule Iwowa adabwa kuti izi zatheka bwanji kuti dzakazi zisike mwachangu choncho, Apa ndi pamene ambili akamba kuti zoonadi zakutsogolo amadziwa ndi Mulungu yekha, science ikuyesela kuti mwina ilosele koma nthawi zonse akumapeza ma number osiyana komanso osagwilizana ndi zomwe anapeza
poyamba.

Kotelo msunso wakula pama samba a mchezo pamene team ya ma researchers yi yomwe ili yaku University ya Radboud ku Netherlands yapeza pa nkhani yolosela tsiku lokutha dziko. Anthu azipembezo zambili sanagwilizane nawo pa chiganizo chi.

Ndipo achenjeza ena kuti asatengele a science kuti akutchula dzaka zosawelengeka, Mulungu atafuna dziko atha kulithesa relo lomwe, komanso olo izi zili chomwe atelo kuti aliyense azikumbukila kuti aziopa tsiku lomwe dziko limakuthela wekha ukamwalira. Kotelo zodikila kuti dziko lithe utha kungopezeka lakutheka wekha. Ndiye Ofunika kuzikonzeleletsa

Atelo ambili ofalisa mawu a Mulungu pamene analetsa za ganizo lakutha kwa dziko

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!