Article
Burna Boy walengeza kuti a mphawi onse asiye kumvela nyimbo zake, pa chifukwa ichi

Burna Boy walengeza kuti a mphawi onse asiye kumvela nyimbo zake, pa chifukwa ichi

Burna Boy walengeza kuti wasiya kuimba nyimbo zosangalatsa a mphawi.

Pamene Oimba Burna Boy akukonzekela kutulusa album yake yatsopano yotchedwa "No Sign of Weakness" wafotokoza kuzela pa Instagram kuti nyimbo zili mu album iyiyi ndi za anthu okhawo amene ali ndi ndalama komanso amakwanisa kugula ma ticket ama show ake.

Akuti onse amaluzi omangomvela nyimbo koma osagula ticket ya show yake, apite azikamvela oimba enawo. Akuti nthawi yosangalasa osauka iyeyu alibe akufuna apange za business basi. Ndipo anapempa kuti uthenga wu osati muone ngati mwano, akungofuna muziwe chilungamo kuti album yi ikatuluka tisamazamve anthu oshota akunena kuti sinawasangalase chifukwa album yi si ya iwowo.

Ndipo anapitiliza kuyankhula, koma tisanapitilize dziwani kuti uthenga osatilawu amafotokozela ma fans ake okhawo a ndalama, ndiye ngati Inu muli gulu la maluzi. Uthenga wanu ndi umene uli mwambawo, pamene uthenga uli munsimu ndi wa okhawo olemela

Burna Boy wayankhula motele kwama fans ake a ndalama " The NO SIGN FOR Weakness TOUR will be different. YOU and I will create our OWN world where only WE exist, EVERY SHOW! Just YOU and Me."

Moti tikunena pano anthu ayamba kale kukalira ku page ya African Giant, kuti Chonde awakhululukile iwowo umphawi sikuti akupangila dala. Komanso ana a sukulu akulira mokweza kuti sanawaganizile pakuti azaiphula pompano. Ndiye kuno ku Malawi ndekuti ife taziwa kale gulu limene ambili tili.

Uthenga ndi umenewo muuzeni nzanu okonda nyimbo za Burna Boy kuti wang'alura ndipo sakutifunanso. Inu mukuonapo bwanji pamenepa, ndi koyenela oimba Kuyankhula ma fans ake choncho?

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!