Article
Vinicius Jr akuti akufuna salary yake isamafanane ndi Mbappe,

Vinicius Jr akuti akufuna salary yake isamafanane ndi Mbappe,

Real Madrid ikuganiza zomusiya Vinicius jnr chifukwa chofuna salary yoposa Mbappe

Vinicius jnr ana sayina contract yokuti akhala ku team ya Real Madrid mpaka chaka cha 2027, wayamba kusintha maganizo kuti akufuna contract yo isinthe kumbali ya malipilo. Ndipo akufuna salary yake ikwele double (X2) kuyelekeza ndi salary ya Mbappe.

Vinicius jnr amene mu contract yake ikukamba zokuti amalandila €14.3 million pa chaka, wanena kuti bola ikhale €25.5 million pa chaka chifukwa achina Mbappe nawo akumalandila ma 14 million ndiye sakuyenela azifanana.

Pa chiganizo chimene chi, akulu akulu a Real Madrid zayamba kumveka kuti mapeto ake angomuchosa ku team Vinicius jnr chifukwa ndalama akukambazo zawachulukila. Zikuoneka kuti ma player aku Brazil sakusangalala ndikubwela kwa Mbappe ku Real Madrid, pakuti Rodrygo naye walengeza kuti akufuna achoke ko ku Madrid chifukwa cha Mbappe yemweyu.

Mbappe yu tsopano tikunena pano ndi amene akutsogola ku zigoli mu La Liga, komanso wadutsa kale Christian Ronaldo pokhala player oyamba kuchinya zigoli zambili mu season yake yoyamba (40 goals).

Kwa inuyo Vinicius Jr ndi Mbappe player amene ali ofunikila kwambili ku Real Madrid ndi ndani?

Admin Jeffrey

Comment Below

6 Comments

Juma

Vini

Cavani Rex

Mbappe

Alli

Onsewo ndi ofnika Ku Real Madrid chfkwa amamenya ma passion osiyana onsewo alibwino pama passion awo Kom a vin angokhala ozimva

Alli

Onsewo ndi ofnika Ku Real Madrid chfkwa amamenya ma passion osiyana onsewo alibwino pama passion awo Kom a vin angokhala ozimva

Happy chikuse

Vin he is better than Mbappe l think Madrid without vinicius 0%

SAMZ

KUWONA KWANGA MBAPE NDI PULEYA WABWINO.VINICIUS JR ALI NDI SANJE KUWONA MMENE MBAPEYU AKUCHITILA

upload your music with us to get maximum reach out!