Article
Koma zomwe zayambikazi ndiye zibwenzi zambiri zithatu

Koma zomwe zayambikazi ndiye zibwenzi zambiri zithatu

Mayi wina wathesa banja lake, chifukwa cha zomwe anauzidwa ndi Chart Gpt.

Mzimayiyu yemwe ndi waku Greece, wathesa Banja lake ndithu, chart Gpt italosela kuti mamuna wake yo ali ndi chibwenzi cha marriage. Chart Gpt yo anachita kufika ponena kuti dzina la chibwenzi cho sangalitchule koma ndi loyambila 'E'.

Izi zachitika pamene Mzimayi yu anagwilitsa ntchito makina otchedwa Chartbot omwe ntchito yake ndikuthazila kuti anthu agule coffee mopweka, ndiye akuti dziko la Greece kuli mchitidwe wa masenga komanso kuombeza omwe amatha kuona zakutsogolo kugwilitsa ntchito zosalira mu coffee kapena mu tea.

Ndiye pakuti chartGPT yu akumathandizila kugula coffee, mayiyu anachiona chanzeru kuti apange maulawo pogwilitsa ntchito zomwe chart Gpt yu akudziwa (pakuti ndi amene amagulira amunake wo coffee). Ndiye chart Gpt sanachedwe koma kulosela zokuti zoonadi mamunakoyo alidi ndi chibwenzi ndipo kutsogoloku amayiwa atsiyidwa.

Apa amayiwa sanachedwe koma kuyamba po za divorce, anthu wa akhala pa banja za ka 12 ndipo ali ndi ana. Ndipo abambowa anayankha kuti aka sikoyamba akazawo wa kutengeka ndi zapa internet, akuti anathesaponso banja mbuyomo chifukwa cha zolosela zina koma patapita masiku anabwelerana.

Koma tikunena pano banja latha ndithu, chart Gpt atawamenyela ma damage

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!