Article
Zaululika kuti Tory Lanez anamangidwa pa mulandu onama, yemwe anaombeladi Megan wapezeka

Zaululika kuti Tory Lanez anamangidwa pa mulandu onama, yemwe anaombeladi Megan wapezeka

Palibe chinthu cha chinsisi pa dziko la pansi, ndipo relo zaululika kuti Tory Lanez anamangidwa pa mulandu onama, yemwe anaombeladi Megan wapezeka.

Pamene zinamveka kuti oimba Tory Lanez wabaidwa ka 14 ali ku Ndende masiku awili apitawo, ndipo tikunena pano ali ku chipatala. Munthu wina wabwela poyela kuzanena kuti Kersey Harris ndi amene anaombela Megan The Stallion ndipo mulandu umene Tory lanez analowela ku ndende ndi omunamizila.

Tory lanez amene anaweluzidwa ndi court kuti akakhale ku ndende kwa zaka 10 koma tsopano bodyguard wa oimba yu wabwera ndi umboni wina omwe waimisa anthu mitu. A Gianno Caldwell afotokoza kuti mulandu wa Tory Lanez unalowa kukondela komanso oweluza ankatengela zokambidwa pa social media, koma no ndi umboni apezawo akukhulupilira kuti wawoyi atuluka ku ndende. Pakuti umboni wu ukukalowanso court

Tikunena pano amene anamubaya ku Nde nde ko wapezeka, komanso ma report kupeleka chikhulupiliro kuti atha kukhala bwino koma mmene ankamupeza atabayidwa anali akukanika kupuma komanso Kuyankhula.

Kotelo ma lawyer tikunena pano akuyesesa kuti akapeza bwino asazabwelerenso ku ndende pakuti umboni okuti sanalakwe wapezeka tsopano. Ndipo ambili akukaikila kuti anthu amene amafuna kumuphawo anali atadziwa kuti Pali kuthekela kokuti Tory Lanez atha kutuluka. Funso kumati Kodi ndi ndani akufunitsitsa kuti oimba yu akhale ku ndende kapena kuti mpaka afe?

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!