Azaumoyo akuti ma minibus driver akumadwala kwambili kuposa ma conductor.
Paja yawo ija ya azamuomoyo akuti pa pakati pa ma minibus driver ndi ma conductor awo, ma driver ndi amene matenda akumawagwila kwambili. Pa anthu 30, ndiye kuti ma driver odwala akumakhala 20 pamene ma conductor odwala akumakhala 10 okha.
Akuti izi zili chomwe chi chifukwa ma driver tsiku lonse amangokhala pamene conductor amakhala busy ku thamanga thamanga, kunyamula Zinthu, kusekula ndi kutseka chitseko mosalekeza, komanso pena kuima kumene. Iwowo anena kuti izi zimathandizila ma conductor kukhala ngati akupanga ma exercise.
Izi azifotokoza ndi a Euan Ashley, wamkulu wa Stanford's Department of Medicine ku mayiko aku ulayako. Atafusidwa kuti Kodi chakudya ndi exercise chomwe chimateteza munthu ku matenda kwambili ndi chiticho. Iwo anena kuti inde chakudya ndi chofunika koma tiziwe kuti zokudya zambili zimakhalanso ndi zinthu zochuluka zosafunika nthupi.
Mwachitsanzo mafuta ambili siawino nthupi Kotelo kuti munthu apewe matenda kweni kweni ndi bwino kuti azipanga exercise, chifukwa amakhala ngati nthupi akulizoloweza kuzuzika ndiye matenda akabwela limawagonjetsa mopweka. Ndiye Iwowa anapelekano chitsanzo cha anthu oyendesa minibus ndi ma conductor kutengela mu study ya 1950 mmene zinkayendela dziko lawo lo.
Komano ku Malawi kuno ndizoonadi kuti ma driver ndima conductor amadwala kwambili ndima driver kuyelekeza ndima conductor? Izo zili apo inu Mukuona kuti exercise ndiyofunikadi kuti muthu apewe matenda? Tisiileni comment munsimu
News source: PBS News
Totally agree 🤝
Exercise ndi ofunika kwambiri I can't say much but i can just say kuti munthu ukamapanga ma exercise umakhala Kuti ukuthamangisa magazi ndikumapangisa kuti thupi lizikhala la mphavu zimene zimapangisa kuti munthu usatenge matenda achisawawa chifukwa limakhala la hot nthawi zonse