Article
Zomavala movula komanso zovala zazitali ngati stima zaletsedwa ku red carpet event ya film festival

Zomavala movula komanso zovala zazitali ngati stima zaletsedwa ku red carpet event ya film festival

Zifukwa zeni zeni zomwe aletsela Zomavala movula komanso zovala zazitali ngati stima zaletsedwa ku red carpet event ya film festival.

Pamene anthu anazolowela Kumavala molaula Kuma event a red carpet, opanga organize ma event wa anena kuti izi zithe chifukwa zayamba kuchotsa ulemu komanso oonela akumayiwala kuti mwambo wo ndi opanga zama filimu ndi kuyamba kukamba za ena mmene anavalira.

Iwowa aweluzanso azimayi omwe amavala zima dress zazitali ngati sitima kuti izi chaka chino ayi, zikumasokoneza anthu ena mayendedwe komanso zikumatha malo okhala. Kotelo amene akuona kuti sakwanitsa zimene zi, basi akhale kwao asapite nawo ku mwambo wu. Akuti zovala choncho azidikila kukakhala ma fashion show ngati MET GALA.

Mwambo wa Cannes film festival ndi umodzi mwa event yomwe ili yaikulu ku nkhani yama filimu, pakuti kumasonkhana anthu opanga ma filimu ochokera kosiyana siyana ndipo kumapelekedwa mphoto zosiyana siyana kuchokera chaka cha 1946.

Ku mwambo wu kumakhala nthawi yozukuta ena mwama filimu a tsopano komanso ma documentaries. Aka sikoyamba oyendesa mwambo wu kuletsa zakavalidwe, chaka cha 2015 analetsa atsikana kuvala nsapato za flat ku mwambo wu. Komanso analesapo azimayi achisilamu Kumavala mozikulungiza nkhope kapena mmutu.

Komano iyi yolesa kuvala molawulayi Mukuona kuti achita bwino

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!