Anyamata awiri omwe anapha makolo awo ku California, court likuganiza zowakhululukila ndikuwatulusa.
Anyamata wa omwe dzina lawo ndi Erik & Lyle Menendez anamangidwa pa mulandu okupha mayi ndi bambo awo ku California Beverly Hills. Ndipo atapha makolo awowa anayesela kuti nkhani ayibise koma therapist wawo ndi amene anapangitsa kuti nkhani iwululike.
Sono zinayenda motele, Anyamata wa anagwilitsa ntchito mifuti kuti aphe makolo awowa ndipo anayesesa kuti zioneke ngati apanga izi ndi akuba chabe ndipo zinathekadi, koma patapita nthawi m'modzi mwaiwo anakamu fotokozera therapist wake kuti anapha makolo awo (paja anthu olemera ati amakafotokoza nkhawa zawo kwa therapist)
Tsopano therapist yo naye mtima posaugwila anakafotokozera ka chibwenzi kake, ndiye chibwenzi cho chitatha nkazi yo anakaulura nkhani yo ku police anyamata wo ndikunjatidwa kuti akakhale ku Ndende moyo wawo onse. Pa nthawi yo anyamata wo wina anali ali ndi Zaka 18, pomwe wina ali ndi Zaka 21.
Tsopano anyamata wa akhala ali ku Ndende tsopano kwa dzaka zothamangila 30, koma kwapezeka umboni okuti Iwowa anapha makolo awowa (makamaka bambo awo) chifukwa chokuti ankawachitila nkhaza komanso kuchita nawo za dama (sexual abuse) osati chifukwa chofuna kulanda chuma chokha ayi. Kotelo court lalengeza kuti koyenela kuti atuluke basi chifukwa akhala mundende zaka zambili kale.
Koma zitengela ngati board yoona za omwe akuyenela kutuluka dzaka zokhala mundende zisanakwane itsimikize. Kotelo alowa mu court kuti akamvetso nkhani yawo (parole hearing) koma lawyer wawo wapeleka chikhulupiliro kuti anthu wa atuluka. Nkhani yawo yi inachitika 1989 ndipo kunatuluka ma filimu komanso ma documentaries ambili okamba nkhani yi, ndiyotchuka ku America ko.
Chochitisa chidwi china m'chakuti ku court ko kunazaza azibale awo akwa bambo awo ndi malemu mayiwa wo kuti akufuna anthu wa atuluke, koma kuli ku Malawi kuno anthu otele achibale angaikileso kumboyo kuti atuluke?
Source : DAILY MAIL
Kumalawi n'zosatheka?nanji Pali ndalama
Kumalawi ndie mzosatheka bro ......achibale ndiwomwe amayambitsa kut akangutuluka tikamutema kunyumbaπ€©
Koma ngati achibalenso akuti atuluke ndiekuti mwina anabisa ndalama amenewo
Eeiissshh Ai ali ndi mwai ndithu mwinad atuluka pajah kwathu kuno ndimpaka ifah moyo wako onse mu ukalavula gaga wanyoo uku kurukuta mano mundende or patapedzeka umbon ngat umeneuπππ
Ndekuti makolo anawonjezadiπ¬
atuluke fast ayamba kukalambatu
Ehhh
Zachamba
Afere komko
Eish... Zovutatu
Zofutatu
Kuli kuno ku Malawi π²πΌ si zingachitike kuti awabakile ayi nanji nanji Pali dollar po aaah ku π²πΌ eeeh amwene ndizina ZINATU kmso pena pake makolowo anafika posafika nawoso sibwino kuti anatibereka okha ndikutipangiraso nkhanza ayi kmsotu ma guy's woo ndekuti anafika potopa cfkwa anapanga zimenezo ingakhale kuti ndneyo singawaphe ayi km ndipita nawo ku police akakhala konko pomwe ndikafunile kukawatulusa akatuluka
Tiuzeni maina ama filimuwo tionere
They are still murderers
So sad kuli kumalawi sangakafikileso kumudzi kwao kuwausa akasake malo kwina
Kkkkk mwamaliza ndi mwanosotu kkkk
Odya zake alibe mulandu my vote π
Afana koma mwakalambatu
Zovutatu..koma atuluke
Chakwera my vote
ππine ndzavotera chakwera
Zovuta
Kwa ineyo akuyenela kutuluka coz ndendeyo ayi njoyisa kwa mbili mix so malem akuchimunawo so amanjoyaso kwa mafanawo yakumbuyo,,,,waiona imeneyo ,,lawyer siwachibwana guyz
Za anthu a chuma Ixi
Lemme write in Chichewa "nkhaniyi ndiomvesa chisoni ndipo ine yandikhuza" π₯Ίπ
Nkhani za serious izi
Yeah kumbali yanga akuyenela kutuluka ndithu zaka zachuluka zedi,komanso ngati mbali zonse ngati achibale aikila umboni kuti atuluke akuyenela kutuluka basi.
Timalakwisa ev day koma Mulungu amatikhululukira
Akuyeneradi kutulutsidwa
Fotseki π
Let's wait for the parole hearing and I have the faith that these two guys are going to be free at last.
Bolatu
Bolatu
Anyamatawa aluyenera unjatidwa
Atuluke inu bodza πΉ
Kuli kumalawi kuno azifuna ndalama kuti atuluke
aaaa zawo izo ππ
Amawanyenga eti
Sad
Zivuta
Ooooh nde nkhan zake kodiπ
Zovutatu
Bambo awo anali ankhanza anayeneraso kulandra nkhanza mxiii kuli kumalawi bwenz atamvekedwa teyala kale kale anawa
Koma bwezi atanena akuwapanga nkhazamo kae..bola chilungamo chadziwika...kuli kuno atawaika mu teyalaa sure
ku America nkhani zimayenda bwino not ku Malawi kuno
OK!!!! π
Ndye mwat amawapakulaso?
Zaziii A Jeffule
Now mwayamba kubweletsa nkhani zabho
Km ndiye zinangovuta kuti samakanena Kwa aliyese Maka pa khaza zomwe amkakumana nazo
It's some fing
Kwathu kuno sanatuluke ndipo sangakukhalire mboni athu akuno eeeπ
Iiiiiiiih kom zina ukamva ππππ
Zosayenda
The justice system is still alive not here in malawi.