Zifukwa zomwe Gabadihno Mhango waisumila Team yake ya ku South Africa kuti impatse 82 Million
Gabadinho Mhango wasumila team yake ya Marumo Gallants ndipo pali chiopsyezo choti atha kumuchosa mu team yo
Nkhani yaikulu ndiyakuti a Mhango atengela ku court team yawo yi ponena kuti yakhala ikugwilitsa ntchito zithunzi zake popanga post pa masamba a mchezo opanda chilolezo Cha iyeyo (violation of image rights)
Akuti team yi imagwilitsa ntchito zithunzi za Gabadinho muma match fixtures, opanda chilolezo kapena gwilizano wa ndalama. Pakuti contract yake sanagwilizane kuti team yi izigwilitsa ntchito zithunzi zake muma promotions awo.
A Gaba afotokoza kuti, kukhala player wa team sikutanthauza kuti akhonza kugwilitsa ntchito dzina lake, ma autographs, initials, nicknames kapena mawu ake muma adverts kapena pa social media opanda gwilizano (pakuti izi ndi zina mwa zinthu zobwelesanso ndalama pazokha)
Iye ananena kuti mphamvu yogwilitsa ntchito zithunzi zake komanso ma signature ake zinali mmanja mwa agent wake ( Prosport) ndipo kwa onse amene afuna kuti agwilitse ntchito zithunzi za Gaba muma advert amayenela kukhala ndi contract komaso mgwirizano wapadeladela.
Kotelo atapita ku team ya Swallows, eni team yi analonjedza kuti agula ma image rights a Gabadinho pa mtengo wa R828 000 koma mpaka lero ndalama yo sanapeleke. Mwina team yi inachitenga chopepuka kupeleka ndalama yi chifukwa tsopano ma image rights wa ali mmanja mwamunuwake Gabadinho Mhango kuchokera 29 August (agency ya Prosport inamusiila)
"Tsopano phindu la image rights, lilino mmanja mwanga" anatelo a Mhango
Sono a Gaba apeza lawyer, ndipo Milandu yi ikuyambila mu December, 2023 pomwe chithunzi cha Gaba chinagwilitsidwa pa fixtures, Kenako video yomwe inaikidwa pa Instagram a Gaba akuyankhulapo za game pa 13 September, 2024. Kumalizila pa 14 March chaka chomwe chino pomwe team yi inapanga share team sheet pomwe panali dzina langa ndi jersey number yanga pomwepo.
Mwachidule a Gaba akuti team yo simayenela kutchula po za a Gabadinho paliponse pokhapokha anakati anapekela ndalama zama image rights anagwilizana zija.
Koma team yo itafusidwa za nkhani yi sinakambeko zokhuza ndalama koma angoyankha moopsyeza a Gabadinho kuti zosumila team yawo zo atha kupezeka alandila nazo chilango mwina so kuchosedwa team kumene.
Source : Sunday World
Achotsedwe koma ampatse zake basi
Hhmmm ndye mukuona kuti tsogoloso losewela mpira kuno lilipo agaba lipitilira eishiiiii zovuta
Athane nawo ikhale example Kwa ma team ena onse
Malawian bwoy no more sleeping.....
Kkkkk zavuta π€£
They should give him money
Ndakaika zoti nkhondo imeneyi aiwina, kmabe ndili pambuyo pako
Amupase ndalam zake katundu wabwno uja sangasowe msika
Azimuchitsa atampatsa zakezo bola
Asawasiye anthu opusa amenewa
Cheteeee ku Stand
We are not sleeping
That legit concern!
Heee owoo,okay Gaba
Gaba akakupasa ndalamazo zibwelako tizadye kunooo
So akulu amhango ndalama izo Mukti zingaperekeka nthena?
The owner of the team he think heβs a cleaver akuona ngat a Malawi we still sleeping
Izizi ngati zili m'malamulo ampira kuti player azilipilidwa chifukwa choti team yagwilitsa ntchito image yake ndekuti basi Gaba amulipire. Zikuoneka kuti ananvana kulipilana koma team ndi imene ikuyenda njomba Wachita bwino kuisumila.
Ndalama aphulire gaba bas
Seems maluzi ayamba kumuyandikira wathuyu, coz sizoona izizi kuti akasumire team yake yomwe, all the clubs wakhala akusewera aja bwanji sankawasumira..anyway it's an issue to do with employer and employee, Mon of my business
Ndeno iyeyo chongofikira kukasuma asadakhale pansi ndi team yakeyo ndichani aa sadaganize bwino apopo
It's his money,so, give to him noow
Aaaaa Gaba diaries Sanakakwitse, ndekut zili mmalemba ampira Akuyenera zake zilowe basi
Ampase iwowo anapangila ndalama iyeyoso adyele basi aaa zikuvuta pati
Aaa π nkhan zake.
Bigger wo adazitaya nkwayeni kumeneko
Ineyo ndimaona ngati gaba azitaye coz zikhonza kubweretsa mavuto pamoyo wake believe me
Gaba walakwisa kwambili akanadekha Kaye wez
Nayeso Gaba ndi Munthu Amafika Potopa π
Ndikuona ngat wachita phuma bwanj
Ndipo agwirisa chithuz chake kopanda chilorezo ndrama iyo mhango amulipire bas kulibe kuchitira mwina
Kalikonse tikamva
Amufumbatisa fupa ena ameneyo
Tingomupempherera Gaba KUT bola 82mitayo ampase kenako no matter amuchotse tisaka kwina kolowera!!
Kalikonse tikaona
I think akudziwa chomwe akuchita
Ine ndikuona ngati apopo olakwa ndi nkazi yo.π
Kwamunthu ngati ineo ndkuona kt gaba wangopeza team ina km akukanika kungotsazika bwnobwno πππ
Kwavutiratu
Gaba alipo wamupopa koma ndikuona ngati sizithsndiza kanthu. Watopa nawo mpira nthawi yake yatha ndiye akufuna apakule papakulu azibwelera kumudzi
I think akudziwa chomwe akuchita chifukwa apo biii palibe team izamufunenso ku RSA powopa azisumilidwa let's pray π kwa pongolin wathu kuti achiphule zosakhetsera thukutazi