DZIKO LA UK LATI SILIPELEKASO VISA KWA ONSE OFUNA KUKAGWILA NCHITO ZA MNYUMBA KOMA OMWE ALI NDI MA DEGREE OKHA
Boma la UK lati likufuna likhwimise malamulo a ntchito mu dziko lawo, kotelo munthu obwela amene aziloledwa kukhala pa ntchito ndi yekhayo amene ali ndi degree.
Izi zasatila pamene ma company amachita kuitanitsa anthu kunja kwa dzikolo pa zintchito zokuti atha kungolemba anthu a konko.
Anthu onse ogwila ntchito za nyumba komanso kusamala okalamba ayamba kuletsa kuwapasa ma visa kuti azipita ku UK ndipo Bomali likuyambatso kuthamangitsa anthu ena kumapita dziko la kwao, pakuti anthu ena obwela wo ali ndi Milandu komanso akumalowa nawo muma program othandizidwa ngati nzika za dziko lo pa ndalama, housing komanso umuyo wabwino (asylum).
Eya akuti ma foreigners ali busy kufuna kulowa mtukula pakhomo waku UK ko komanso kufuna kukhala ma citizen (2 Million immigrants claiming citizenship each year) ndipo izi zakwiyisa boma lakumeneko. Kotelo akuti ngati unapitila sukulu usapezeke ukugwila ntchito za nyumba pokhapokha ulembedwe ntchito yogwilizana ndi degree yako, kupanda apo azikuthamangitsa.
Mayiko ngati Nigeria, Pakistan ndi Sri Lanka ndi ena mwa mayiko amene akuti akunyanya pa mchitidwe wu, ndiye boma la UK lati inde malamulowa agwila ntchito kwama foreigner onse koma mayiko atatu awowo Nde azichita ku wapanga target.
Malawi ikuoneka ndi mbili yake ya khalidwe labwino mwina litipulumusa, chifukwa ma lawyer ena akumenyela ufulu ku UK Komwe akuti khalidwe likufuna lichitikeli ndilosalana. Koma ngati izi zingakhale chomwe chi anthu ayeneleka kusamala ndipo kwatuluka kanema wina yofotokoza mmene mungapewele kuphinjika ndi malamulowa.
Watch https://vm.tiktok.com/ZMSejCgdW/
Source : LBC & Sky News
Eeeh zovuta ndthu 😫
Kwavuta