America yatsitsa tsopano misonkho ya katundu wa ku China (Tarrifs), ataona mavuto amene izi zabweletsa.
America alengeza tsopano kuti yagwilizana ndi China kuti atsitse misonkho yomwe anaikilana akafuna kupanga malonda. Misonkho yi yomwe dzina lake ndima Tarrifs, boma la America linakweza mpaka kufika pa 145% pa katundu ochokera ku China. Mwachitsanzo ndekuti katundu amene anali wa $100, kumupasa ma tarriff a 145% ndiye kuti afika pa $245. Izi zinapangitsa kudhula kwa katundu ndipo ma business ambili anangosiya kugula katundu waku China yo.
Sono zinali zovuta kuti America ingakhale opanda katundu waku China, chifukwa zinthu zambili zimachokela komweko. Ndiye anthu a business ambili anadandaula kuti izi zikapitilira za misonkhozi zinthu zambili mma shop sizimapezeka.
Ndiye kucha kwa relo America yachepetsa misonkho yake kuchoka pa 140% kufika 30%, ndipo nayo China yachepesa misonkho yomwe inaika kuchoka pa 125% kufika 10%. Koma akuti izi zichitika kwama tsiku 90 okha pokhapokha mayiko awili wa apange chiganizo chomveka bwino, pakuti izi zangochitika mogwilizila.
Izi zikupitiliza kuonetselatu kuti Boma la a Trump likupanga zambili lisanaganize mokuya pa ziphinjo zomwe zingabwele paziganizo zawo. Ndipo zikuyembekezelekaso kuti America yi isisa misonkho yomwe ina ika ku mayiko onse kutengela mmene atakambilane