Article
Zoona zenizeni zomwe President Putin anawaitanila a Ibrahim Traore kuti akakambilane ku Russia

Zoona zenizeni zomwe President Putin anawaitanila a Ibrahim Traore kuti akakambilane ku Russia

Ibrahim Traore tsopano anakakumana ndi president waku Russia Putin, anthu atutumuka ndi zokambilana zawo zili munsizi

Ibrahim Traore amene ali msilikali komanso president waku Burkina Faso tsopano wakumana ndi president waku Russia Vladimir Putin. Ndipo pa mkumano pawo Russia inachita kutumiza ndege za mtundu ka jet zokuti zimuteteze pa ulendo wu. Ndipo zolinga za mkumano wu zinali zotele;

Putin anatsegulira ndi Kuyankhula kuti ndi osangalala ku waona a Traore maso ndi maso, ndipo anachitenga cha mtengo wapatali kuti analora di kupita ku Russia pakuti awili wa ndi azitsogoleri amene atchuka tsopano ndi kulimba mtima komanso osamala zokhazo zofunikila kwa anthu amayiko awo okha posatengela kuti mayiko ena akuti chani.

Awiliwa zikumveka kuti anakumanaponso mu 2023 kumene a Putin anathandiza maganizo a Traore pa nkhani za ndale atapita ku meeting yomwe inali pakati pa Russia ndi mayiko amu Africa. Koma ulendo uno anakumana pa mwambo umene Russia ikukumbukila anthu amene amenyela ufulu kudzera mu nkhondo (80th Anniversary of victory in great patriotic war)

A Putin anapitiliza kunena kuti awiriwa ndi ofanana pakuonesesa kuti akumenyana ndi kuthana ndi onse achiwembu komanso ofuna ku wa bwenzeletsa mbuyo. Ndipo akuti ndi koyenela awili wa kuti azithandizana ku nkhani za chuma komanso zamalonda. Ndipo alonjedzatso kuti athandizila kuphunzila ulere ana aku Burkina Faso okwana 3,500 pa chaka.

Kuphatikizila apo Russia ithandizilanso kutukula umoyo wabwino mu dziko la a Traore. Izi zikuphatikiza kuwamangila ma laboratory komanso kuphunzitsa ma dotolo. Akuti chaka chatha anatumiza chakudya ku Burkina Faso chokwana 25,000 tonnes ndipo chaka chino atumizaso chambili (wheat).

Ndipo mawu ambili a Ibrahim Traore kunali kothokoza koposa, ndipo alonjedza kuti aonetsetsa ubale umenewu ukhale wabwino chifukwa uwapindulira zambili ku umuyo wa anthu aku Burkina Faso.

Meeting imeneyi yayika mayiko ena ambili pa mpanipani, kupangila kuti panali mayiko ambili aku Europe komanso America amene samawaonela kukodwa a Traore ndipo apulumuka kangapo ku ziwembu zofuna kuphedwa. Mokuti ubale umenewu uthandidzila mtsogoleri waku Burkina Faso kutetezeka chifukwa zikuoneka wapeza m'bale oyenela. Tiona kuti zitha bwanji

Source: 80 news
http://en.kremlin.ru/events/president/news/76895

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!