Article
Trump akuti Azungu onse aku South Africa azipita ku America ngati ma refugees, iwo ati zifukwa zake ndi izi:

Trump akuti Azungu onse aku South Africa azipita ku America ngati ma refugees, iwo ati zifukwa zake ndi izi:

"Azungu onse aku South Africa azipita ku America ngati ma refugees " latelo boma la America

Pamene Bola la America lakhala busy ndi kuthamangitsa anthu obwela kuti a zipita kwawo, pali gulu limodzi limene anena kuti akulifuna kuti lizipita ku Amerika. Anthu amene wa ndi azungu aku South Africa ( white Afrikaners)

Dziko la America tikunena pano likulonjedza kuti azungu aku South Africa wa, aziwa sunga ngati ma refugees koma awakonzera kale ma nyumba oti azikakhala, ndipo mumanyumbamo muli ziwiya zongoyambila chabe, komanso ndi tizida togwilira ntchito kukonzera pakhomo, osaiwala so ma groceries, zovala ndi ma phone oimbila ulere.

Funso m'kumati m'chifukwa chani anthu amene akulandila special treatment imeneyi ku dziko la America? Chona cheni cheni ndi chakuti a Trump akhala akuonetsa chidwi za anthu amene kwaka nthawi ndithu , kufikila pokuti dziko lawo litasiya Kuthandiza ma refugees ambili lasankhabe ku sunga chithumba chothandiza azungu aku South Africa wa.

Anthu wa sikuti ali pa umphawi kapena mavuto ali onse. Koma dziko la America langoona kuti ndichanzeru kuti azikawaonela pafupi anthu agulu li, ndipo ma report akuonesa kuti boma lawo lakhala likukonzekela dongosolo li kwaka nthawi panopa.

Mwachidule nkhani siyofuna kuthandiza ma refugees, koma akufuna anthu a chizungu azikhala mowandikana nawo ku Amerika konko. Chifukwa tikamati ma refugees nthawi zambili timanena anthu omwe akhunzidwa ndi zinthu ngati njala, nkhondo, chilala, kapena kuzuzidwa kwa njila ili yonse. "Pamene izi zikuona kuti ndi njila yongofuna kusamala kakhalidwe ka azungu" watelo analyst 'Kaitlyn Hennessy' yemwe ndi m'zimayiso wa chizungu koma sanagwilizana ndi mfundozi.


Source : Katy Tur

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!