A Science akuti azindikila mtundu wina wa anthu omwe tulo la 4hrs ndi lokwana osati mpaka 6hrs.
Pamene a science omwe akhala akulengedza kuti munthu amayeneleka kumagona ma ola osachepela 6hrs, lero abwelanso ndi nkhani ina akuti pali gulu lina lomwe litha kumagona 4 hours yokha opanda kudwala mthenda zomwe zima bwela chifukwa cha kusagona kokwanila kapena kugona kopitilira myezo
Iwo sakulesa zokuti anthu azigona ma hours ambili zija ayi koma akuti pamene anthu ambili akufunikila kumagona 7 to 9 hours kuti asadwale matenda ngati Alzheimer komanso matenda ena a mtima Paliso gulu lina lomwe kugona 4 hours yokha singadwale zonsezo.
Funso mkumati ungaziwe bwanji kuti uli gulu logona 4 hours lo? Omwe azindikila izi ndi anthu ofufuza za umoyo wabwino ku Chinese Academy of Science akuti anthu Ofunika kugona nthawi yochepa wa akuwatchula kuti ali ndi 'Mutation function' ndipo akuti anthu amene wa akagonetsa amazimva ngati akudwala akamadzuka kapena mutu kupweteka kumene
Pamene a Malawi ena amva izi akuti kugona kwambili ndikusaziwa mavuto, zomwe akuti apeza a science a ku china zo iwo anaziziwa kale kale ndipo si nkhani ya yachilendo