Article
Trump wathetsa nkhondo ya India ndi Pakistan, ndipo njila imene wagwilitsa ntchito ndiyotele:-

Trump wathetsa nkhondo ya India ndi Pakistan, ndipo njila imene wagwilitsa ntchito ndiyotele:-

Trump wathesa nkhondo yomwe Inalipo pakati pa India ndi Pakistan. Kodi izi zatheka bwanji?

Zikuchitika pompano, a Donald Trump alengeza kuti anakhala pansi ndi mayiko wa ndipo agwilizana kuti nkhondo yomwe inali pakati pa India ndi Pakistan yatha tsopano.

A Trump akuti izi sizinali zopweka chifukwa zatenge la Iwowa usiku onse akukambilana ndi akulu akulu amayikowa kuti afike povomeleza kuti nkhondo yi ayithesedi. Ndipo apitiliza ndikuthokoza mayikowa pa chiganizo chi.

Ichi ndi chizindikilo Chimodzi chokuti president Trump samakonda nkhondo ndipo aka sikoyamba ku muona akuyesesa kuti nkhondo ithe, pakuti ngakhale nkhondo ya Russia ndi Ukraine akuyesesabe kuti aithese. Ambili atamanda A Trump pa mtima umenewo.

Uthenga wu watulusidwa kudzera nyumba ya ma uthenga yotchedwa #TruthSocial. Ndipo kwa omwe samadziwa za nkhondo yomwe inali po pakati pa mayikowa,

Dziwani kuti dziko la India ndi Pakistan linayamba udani wake kuchokera kale kale kwambili, Poyamba mayikowa anali dziko limodzi ndipo anagawanikana mu chaka cha 1947. India linakhala dziko la chi hindu kwambili pamene Pakistan kukhala dziko la chisilamu.

Awiliwa akhala akukangana pa nkhani zachipembedzo komanso ndale ndipo masiku awili apitawo anayamba kuponyela na mabomba. Ndipo tsatane tsatane wa mmene nkhondo yi anachitikila,


Welengani article yomwe inafotokoza bwino lomwe munsimu.

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!