Article
Nkhondo ya India ndi Pakistan yayambika, koma mayiko onsewa sakunena chilungamo ichi:-

Nkhondo ya India ndi Pakistan yayambika, koma mayiko onsewa sakunena chilungamo ichi:-

NKHONDO YA INDIA NDI PAKISTAN YACHULUKA BODZA.

Pamene ubale wa dzilo la Pakistan ndi India wakhala oipa kwa dzaka zochuluka, tsopano kwayambika nkhondo ndipo tikunena pano ayamba kale kuphulitsana komanso ziwembu koma, zomwe zadabwitsa ndi izi:

Masiku awili apitawo, dziko la India linakaphulitsa dziko la Pakistan Malo 9 ndipo dziko la Pakistan nalo labwenza kuphulisa (kwambili akungophulitsana muma site a military) . Koma chodabwitsa m'chakuti mayiko onsewa akumapeleka ma report okaikisa penanso onama ku news.

Mwachitsanzo Pakistan ikumane zaboza zomwe India yachita, komanso India kunena zosiyana pa zomwe zachita kapena kuchitilidwa. Nkhani yaikulu dziko lililonse likufuna kuoneka kuchenjera pa zomwe zikuchitika komanso kufuna kuonesa anthu awo kuti asadandaule zonse zili bwino bwino.

Chikuopya chakuti mayiko onsewa ali ndi zida za Nuclear ndipo wina akangoganiza kuyamba kuzigwilitsa ntchito kukhala anthu ambili okhuzidwa kupangila kuti, inde pano anthu akuvulara komanso ena kumwalira koma si ambili, kutengela kuti onse akumapanga attack ma military sites.

Mukuona kuti ndi zoyenela mayiko wa kumanamidza anthu awo kuti asamadandaule kapena kuopa?

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!