MBIRI YAYAMBA KUMVEKA KUTI PAPA WA TSOPANO YI SAMAGWILIZANA NDI A TRUMP.
Izi zayamba kuzungulira kutengela zimene Papa watsopano yi wakhala akulemba pama tsamba ake a mchezo pa nkhani zokhuza ulamuliro wa a Trump.
Papa wa tsopano amene wangosankhidwa dzulo dzina lake ndi Robert Prevost ndipo ndi papa oyamba kukhala ochokera ku Amerika. Ambili anali oyembekezera kuti President wa America a Trump ndiye kuti akhala phatiphati ndi Papa yi, koma zomwe anthu akapeza ku page ya papa zaimitsa mutu ambili.
Ma post analembedwa papa yu asanasankhidwe, amakamba zambili zokhumudwa ndi mmene a Trump akuyendetsela dziko makamaka pa nkhani zothamangitsa anthu obwela mwachisawawa komanso anazuzulaso vice president wa trump wo.
Ma post amene atchuka wo anali olimbikitsa kuti ndi bwino tonse tizikondana ngati anthu osasankhana mayiko, kupangila kuti njila imene Trump amagwilitsa ntchito kuthamangitsa anthu mu dziko la America inali yozunza.
Ambili akambako kuti mwina izi papa yo ankayankhula chifukwa naye wakulira komanso kugwila ntchito mayiko achilendo Ngati Peru komanso Italy, ndiye amaone kuti sizoyenela kumauza anthu obwela.
Ndiye pakuti Papa amaloweleranso nkhani za ndale, ambili ayamba kukhala ndi chikhulupiliro kuti mwina athandizila kumuchepesa moto Trump pa makhalidwe ake ena omwe ambili sakugwilizana nazo.
Source: Daily Mail