MPIKISANO OWONA KUTI MA SPERM ACHANGU NDI A NDANI (SPERM RACE) , WACHITIKA KOYAMBA KU AMERICA
Ana a sukulu ku dziko la America ku Los Angeles anapangitsa mpikisano ofuna kuona kuti Kodi amene ali ndima sperm a changu ndi ndani? Kupangila kuti ati kuti munthu apeleke mimba ma sperm ake othamanga kwambili ndi amene amasanduka mwana.
Iwowa akuti chiwelengelo cha anyamata osabeleka chayamba kuchuluka ku America ko ndiye ndalama zomwe atolera pa mpikisano wu zithandizila kuthana ndi vuto li. Tsopano mpikisano wu unayenda chonchi:-
Anthu amene amapikisana anali a nyamata awili, ndipo anatenga ma sperm awo (sitikudziwa kuti anatenga bwanji) koma atawatenga anawaika mu nsewu changati microscope chomwe chinakonzedwa ngati njila yomwe ma sperm wa azipikisanamo
(Kumapeto kwa njila yo kunali kooneka ngati reproductive system ya azimayi).
Munthu otchedwa "Tristan milker" ndi amene anawina mpikisano wu ndipo watchulidwa kuti "Fertility Athlete". Mpikisano wu anthu anauwonela live ndipo akuti mpaka ena ana Betta.
Amene anakonza mwambowu alengeza kuti akwanitsa kupeza ndalama yokwana 1.4 million USD kudzera mu mpikisano wu. Ndiye kuti mwina owina akumadyapo so osalephera, pa chifukwa ichi a Malawi ambili apempha kuti izi zifikenso ku Malawi iwo ali okonzeka ku wina