Article
Kodi mpaka zimafikaso apa akamalumbilisa papa?

Kodi mpaka zimafikaso apa akamalumbilisa papa?

Zodabwisa zimene zikuchitika ku mwambo olumbilisa Papa madzulo ano

Pamene dziko lonse limayembekezela mwa chidwi kuti zisankho zosankha Papa ziyenda bwanji, zatsimikizika kuti tsopano Papa wapezeka ndipo dzina lake ndi Robert Prevost koma akhala akutenga dzina lokuti Papa Leo XIV.

Anthu anali okodwa pamene anangoona utsi wa white ukutuluka phindi zapitazo, kutengela kuti utsi wu umakhala chizindikilo chokuti Papa wapezeka. Tsopano dziwani izi zokhuza papa watsopano yi komanso zodabwisa zina zochititsa chidwi zomwe zikuchitika ku mwambo olumbilisa papa madzulo omwe ano

Aka ndi koyamba Papa kukhala ochokela dziko la America, ndipo a Robert Prevost ndi a dzaka 69 zakubadwa (Born in Chicago 1955). Iwowa agwila ntchito yawo yambili mu dziko la Peru (South America) ndipo mu chaka cha 2023 iwowo anagwilaponso ntchito ndi Pope Francis amene wangotisiya kumene yu.

Chodabwitsa china chomwe chinachitika utsi oyelawu usanatuluke, chinali chokuti ka mbalame kanatuluka pa denga pomwe anthu amaonelapo utsi, (ena akuti ichi chinali chitsimikidzo chokuti kwabadwa ulamuliro wa tsopano)

Papa wa watsopano yu akhala wachi namba 267th ndipo kufika tsiku la relo akhilistu achi Katolika alipo okwana 1.4 billion dziko lonse (obatizidwa okhaokha). Ndipo iye waonekela kugulu ndiku ya khula mawu okuti "mtendele ukhale ndinu nonse" ndipo wapelekaso ulemu ku papa Francis amene wamwalira mwezi wathawu.

Source: Fox News

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!