Article
Koma inu mwati Kanye West tsiku lina sazavula Mbulanda uyu?

Koma inu mwati Kanye West tsiku lina sazavula Mbulanda uyu?

KANYE WEST SAKUFUNIKA PA SOCIAL MEDIA, WATELO PIERS MORGAN PA ZIFUKWA IZI:-

Kutengela zomwe Kanye west anachita komanso kuyankha pa interview imene Inalipo dzulo ndi Piers Morgan, ambili ayamba kudabwa ngati Kanye yu ali wa bwino bwino kapena ndi misala.

Khaliwe la Kanye west lakhala likupitilira kwaka nthawi pa nthenda imene ili ya Bipolar, ndiye amakhala ngati misala yochita kukhala ndi season. Ena ambili achita kufika pomuzolowela pa zomwe amayankhula pamene ena akuti amachita dala.

Mwachitsanzo, dzulo anali pa interview ndi Piers Morgan yu yomwe cholinga chake chinali chinali chokamba zokhuza album ya new one yotchedwa "Donda 2". Ndiye atamba ku mufusa kuti ali bwanji, zinayambila pomwepo kuyankha zosiyana, akati kuyamba kutchula za Michael Jackson ndi zambili zokuti sanafusidwe. Mpaka anangochokapo osamaliza interview.

Ndiye kutengela zonyoza zomwe wakhala akulemba pa masamba ake a mchezo, kukamba zolaula. A Piers anaona kuti ndi bwino Kanye ngati zingatheke achosedwe Kaye pa social media kuti azitolere, pamene ena akuti iyayi Kanye yu panopa amapangila dala for attention. Inu muli mbali iti?

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!