TRUMP WATI AKUFUNA AGULE DZIKO LA CANADA, NDIPO WAOPYEZA IZI
Donald Trump amene ali President wa dziko la America anayankhulapo masiku a m'mbuyo mo kuti ali ndi khumbo lofuna dziko la Canada liphatikidzane ndi dziko la America. Ambili amaona ngati ndi nkhamba kamwa chabe koma zadabwitsa anthu kuona kuti Prime Minister waku Canada anapita ku America kukakambilana za nkhani yi.
Canada ndi dziko limene lili mu malire ndi dziko la America, kotelo a Trump akuti ndi koyenela kuti mayiko wa akhale dziko limodzi, kapena kuti Canada ikhale state ya America yachi 51. Trump anena kuti Canada imadalira Zinthu zambili ku America monga chitetezo komanso nkhani za Malonda.
Ndipo Prime Minister waku Canada a Mark Caeney anavomeleza ndithu kuti ndi zovuta kuti Canada iyendese Boma opanda thandizo la America, komabe iwo ananenetsa kuti dziko lawo silogulitsa ndipo zomwe akunena a Trump sizingatheke. Koma a Trump akuti palibe chosatheka.
Ndiye a Trump anaopyeza kuti dziko lawo lisiya pompano kudalira zokudya, ma galimoto, komanso ma minerals aliwonse ochokela ku Canada chifukwa America ili ndi kuthekela kozipangila zonse zi pa zokha. Ndipo anena so kuti awakwezela ma tarriff komanso misonkho akafuna kulowesa katundu mu dziko lawo.
Mwachidule ambili anafotokoza kuti a Trump anayankhula monyazisa Prime minister amene anali naye meeting masiku apitawa. Inu mukuona kuti ndi zotheka kuti dziko ngati Canada ndikugulidwa ndithu
Sizoona kt dziko ngati Canada likagulitsidwe