Article
Zodabwisa Zina zimene akuchita azimayi lero ku Vatican pamene akupitiliza kusankha Papa

Zodabwisa Zina zimene akuchita azimayi lero ku Vatican pamene akupitiliza kusankha Papa

Azimayi a Katolika ayamba kupanga ma demo okuti nawo azikhalapo posankha Papa ku Vatican

Zodabwisa Zina zimene akuchita azimayi lero ku Vatican pamene akupitiliza kusankha Papa

Pamene dongosolo losankha Papa lili mkati, azimayi ena otchedwa 'International group Of Women's Ordination Advocates' ayamba po kupanga ma demo akuti si zoona kuti azikhala azibambo okha posankha papa pamene mpingo ndi wa aliyense.

Iwo akuti sakukhutila ndi zokuti azibambo okwana 133 angapeleke chiganizo chabwino opanda azimayi, amene ali half ya population ya church cha Catholic.

Ndiye tikunena pano ali panja pa Vatican, komweko Komwe kukuchitika mwambo osankha papa komweko kupempha akulu akulu a church cha Katolika kuti apange po kanthu mwa changu.

Pama demonstrations awowa iwo akugwilitsa ntchito utsi wa pink ati kusonyoza chikhulupiliro kuti zitheka komanso kutanthauza kuti akwiya ndipo akufuna kuti pempho lawo liyankhidwe changu kuti alowe mu Conclave akasankhe nawo papa. Ndipo iwo ati akuimilira azimayi ambili omwe akudandaula kunjako.

Ngakhale azimayi anzawo ena akana kupanga support zimenezi, azimayi wa anenetsa kuti iwo ndi a Katolika ndithu ndipo sakuonapo vuto.

Source: RTE News

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!