Zodabwisa zimene zimachitika ndi ma Team a mu Champions League Papa akamwalira chaka chimenecho
Pamene UEFA Champions League ili Kuma semi finals, relo kuli game ya Arsenal vs PSG (9:00 PM) ndipo amene atawine ndi amene apite ku finals. Koma mbili ikuonesa kuti Arsenal ili ndi mwayi ofika finals mpaka kutenga chikho, chifukwa cha ku mwalira kwa Papa Francis.
Izi zili chomwechi kutengela mbili yomwe akuti, chaka chilichonse chomwe Papa wa mwalira team yaku England ndi imene imatenga chikho cha Champions league.
Mwachitsanzo Papa John Paul atamwalira 1978 Nottingham Forest yaku England ndi imene inatenga Champions League, Kenako so Papa John Paul (II) atamwalira 2005 Liverpool ndi imene inawina UCL. Sizinathele pomwepo chaka cha 2022 Papa Benedict 16Th atamwalira Manchester City ndi imene inawina chikho chimenechi cha Champions league.
Nde potengela kuti chaka chino Papa Francis ndi amene wamwalira, ndiye Arsenal kukhala team yokha yo yaku England yomwe yasala mu mpikisano umene wu. Olosela angomalizitsa kuti owina amudziwa kale basi.
Ndiye zoona zenizeni tiziona kuyambila pa game yomwe ilipo madzulo ano, pamene Arsenal ikumenya ndi PSG. Inu Mukuona kuti zimenezi zithandizila ma Gunners kuwinadi championships league?
Mbili ikuonesa kuti Arsenal sinawinepo UEFA Champions League, ndipo inafikapo kamodzi kokha muma finals mu chaka cha 2006 (Nthawi ya achina Thierry Henry). Kotelo ngati ingawine aka kakhala koyamba.
Koma nkhani ndiya kuti Papa Francis ali nawo ndithu a Arsenal pa ulendo wu. Inu muli mbali iti?