KULUZA KWA BARCELONA FC DZULO, NDI MINYAMA YA LAMINE YAMAL IJA?
Dzulo team ya Barcelona yaluza 4 kwa 3, pa masewelo amene analipo ndi team ya Inter Milan mu ndine ya Semi-finals ya UEFA Champions League.
Pamapeto a game yi ma player ambili a Barcelona analira misonzi ngati ana posakhulupilira zaku gonjaku. Koma ndi chifukwa ninji ma fans ena pa social media ayambapo kuloza dzala Lamine Yamal?
A Lamine Yamal ndi player wa team ya Barcelona amene ali wa zaka 17, kufika pano wasewela ma games okwana 104 ndipo wakhala player ofunikila ku team pogoletsa komanso kuthandidzila zigoli. Potengela kuchepa kwa msikhu wake ambili anayamba kumufanizila ndi Leo Messi amene naye anasewelepo team yi kuyambila ali wachichepela.
Koma zinthu zinayamba kutembenuka ndipo anthu ena anayambapo kutchula player yu wa mwano pazimene Lamine Yamal anayankha atadzudzulidwa pazina zomwe anachita komanso kuvala atawina chikho cha Copa Del Rey. Iye anayankha kuti "oluza sangamuuze chochita"
Ndiye kutengela kuluza kwa team yawo dzulo, anthu pa internet anakumbukila mawuwa, kusatila kuti Barcelona yaluza mwayi ofika finals ya UEFA CHAMPIONS LEAGUE zomwe ambili amayembekezera kuti ali ndi mwayi waukulu owina chikhochi.
Nkhani yabwino posatengela kugonja kwao a Barcelona, player wawo Raphinha wafanana ndi Christian Ronaldo pa mbili ya anthu ogoletsa komanso kuthandidzila zigoli mu season imodzi ya UEFA Champions League (Most goal involved in UCL season)
Inu Mukuona kuti anga wine ndi ndani chikho chimenechi pamene Barcelona yaluza? Madzulo ano kuli game ya Arsenal ndi PSG kuti papezeke yemwe atapite ku finals kukamenya ndi Inter Milan.