Zodabwisa zimene zitachitike pa mwambo osankha Papa omwe ukuyamba lero
Kusatila ku mwalira kwa Pope Francis pa 26 April, 2025. Relo pa 7 May ndi tsiku loyamba pa mkumano osankha yemwe angakhale papa watsopano (conclave) ku Vatican church chotchedwa Sistine Chapel.
Chomwe chadwabwitsa komanso kutsangalatsa ambili ndi kumva kuti pa list ya omwe angasankhidwe kukhala Papa palinso anthu aku Africa, zomwe pali chiyembekedzo chokuti mwina Papa ndi kukhala waku Africa. Izi zili chomwe chi pa zifukwa zingapo izi👇
Papa Francis asanamwalire, anasintha ena mwama lamulo pofotokoza kuti ndikoyenela kuti ma cardinals azisankhidwa mayiko osiyana siyana kuti mwina pazikhala maganizo okomela mbali zonse za dziko lapansi (ma Cardinals ndi anthu amene amakhala ndi kuthekela kokhala Papa)
Masiku ambuyomo ma cardinals wa amakhalapo 120 koma pa zisankho za relo ma cardinals amene afika ku Vatican akwana 133 pamene ena awili sanakwanitse kukhala nawo chifukwa cha matenda. Kotelo munthu amene akuyeneleka kukhala Papa afunikila ma vote okwana 89 kuchokera kwama cardinals a zake kuti akhale papa.
Tsono dziwani zina zochititsa chidwi komanso ndondomeko yomwe imachitika posankha Papa; Choyamba dziwani kuti zisankhozi zimakhala za chinsisi, 2. Ma cardinals onse amalandidwa ma phone komanso samaloledwa kumva zomwe zikuchitika panja kudzela pa news, TV ngakhale radio, 3. Anthu amene ali panja amaonela utsi kuti aziwe zomwe zikuchitika mu zisankhozi, Mwachitsanzo ngati utsi utatuluke wa black ndekuti ndi chizindikilo chokuti papa sanapezeke koma ngati utsi utatuluke wa white ndiye kuti Papa wasankhidwa.
Zisankhozi zilibe nthawi yoyikika, koma mbuyomu ma papa amasankhidwa pa matsiku awili kapena atatu, koma ngati owina sakupezeka zimapitilirabe mpaka ma week. Ma cardinals wa ndi amene amasankhana okhaokha kukhala Papa koma samaloledwa kuzivotela okha.
Mmene mo ndi mmene zikuyendela nkhani zosankha Papa, funso mkumat; Inu mungakonde Papa atsankhidwa waku Africa?
Onelani list ya anthu amene ambili akuganizila kuti angakhale papa mu video ili mmusiyi👇
Link : https://youtu.be/5oBl53X4OL0?si=VN6sVh66crF-taKo