President Trump wawayankha Mwano a mpingo wa Katolika atamuzuzula pamene anaika picture yozifanizira ngati Papa
President wa America a Donald Trump anazuzulidwa ndi a mpingo wa chikatolika pa zomwe anaika pa tsamba lawo la mchezo masiku awili apitawo (PA 4 May)
A Trump anaika chithunzi choonesa iwowo atavala ngati Papa, ndikumanena kuti inde ali ndi khumbo lofuna kukhala papa kusatila kumwalira kwa Pope Francis. Ndipo izi zinakwiisa a mpingo wa katolika ndipo anachitenga ngati akunyoza kutengela kuti ndondomeko yomwe imafunika kukhala papa a Trump palibepo.
Dzulo a Trump aonjezelaso kuyankha mwachibwana atafusidwa kuti maganizo awo ndi otani kusatila kukwiya kwa ma catholic pa picture yomwe ndiya Al generated koma inapangidwa share pa page pawo komanso pa page ya White house, ndipo iwo ayankha mtima uzi zii kuti
“Vuto lake a Katolika wa sakutha kuona kuti inali joke chabe (iwo akuti amangopanga zosewela) kuphatikizila apo iwo akuti si vuto lawo chifukwa chithunzi cho anangochipezaso pa internet anachipanga si iwowo. Ndipo a aonjezelaso kunena kuti ma catholic eni eni chithunzi cho chinasangalatsa akukwiya wo ndi anthu amabodza chabe.
Sanathele pomwepo, anatinso akazawo a trump akuti chithunzi cho anachikonda kwambili ngakhale iwo a Trump wo amasuka no kunena kuti sangafune kukhala Papa chifukwa samakwatila, iwo akuti pokhapo Nde pamene panabwenza mbuyo atamva kuti papa sakwatila.
Mwachidule a Trump sakuonapo vuto lililonse, ndipo akuti kwao izi ndi zocheza amene waona vuto amene yo ndi amene ali ndi vuto, ndipo tiyembekezere ma joke ambili ku page kwao komanso page ya White House apapa wangoyamba chabe