Article
Mulandu wa P-Diddy unalowa mu court koyamba dzulo, Ndipo kwachitika zodabwisa izi

Mulandu wa P-Diddy unalowa mu court koyamba dzulo, Ndipo kwachitika zodabwisa izi

Mulandu wa P-Diddy unalowa mu court koyamba dzulo, Ndipo kwachitika zodabwisa izi

Sean Diddy Combs amene ali munthu otchuka kwambili ngati oimba wa chamba cha Hip Hop komanso ngati munthu wa business ku Amerika anamangidwa miyezi 7 yapitayo pa Milandu yoposa 100

Dzulo pa 5 May kanali koyamba kulowa court kuti amugamule pa Milandu yomwe akumuganizilayi Ndipo pachifukwa choti Milandu yachulukitsa dzulo court linayamba ndi kumuzenga ma criminal charges amene akukhunza Milandu yake monga 1. Racketeering Conspiracy 2. Sex trafficking 3. Transportation for prostitution ndipo iye anayankha kuti

Ndi osalakwa, pachifukwa chimenecho mulandu wake upita ku trial yomwe ifunika ochitila umboni (jury) yomwe imakhala anthu 12. Koma izi zomwe zili zochitisa chidwi

Anthu anachita kugona panja pa court kuti asunge Malo komanso kukhaliratu pa line yokalowa mu court, ndipo omwe anachedwa amachita kuwagula Malo omwe anafika kale kale kuti asinthane, moti ena aiphula kumeneko chifukwa chogulisa Malo awo akutsogolo pa line yolowa mu court kukamvela mulandu wa P Diddy.

Mulandu wu akuletsa kujambula, koma amene anakwanitsa kulowa anafotokoza kuti maonekedwa a P Diddy kuti akumvetsa chisoni kwambili, tsitsi lawo lonse labwela white (invi) zomwe sizinkaoneka asanamangidwa, komanso anaimisa mulandu kaye kuti akataye madzi pakuti akuti anali ndi mantha. PA Milandu yonse yi akapezeka olakwa chigamulo chake ndi cha kuti akakhala ku ndende moyo wawo onse.

Sono dziwani izi zokhuza Milandu, Mulandu umene jury kapena kuti mboni 12 zimafunika kuti zithandizile kuzenga mulandu, zimafunika akhale anthu okhawo amene akudziwikilatu kuti apeleka chiweluzo kapena judgement yosakondela. Ndiye potengela kuti a Diddy ndi munthu otchuka komanso ambili anamva kale za mulandu wawo zikhala, zovuta court kusankha anthu oyenela kupangila ma lamulo Amati ; mboni kapena kuti jury zimakhala bwino akhale kuti sakumudzi yemwe akuzengedwa mulandu.

Ndiye kuli ka ndondomeko Komwe kakusatidwa, koma zayamba kale kumveka mphekesela kuti anthu ambili amene akusankhidwa kuti amvetsele komanso kuthandidzila kupeleka chigamulo akudziwa kale za mulandu wu komanso anaonapo video yomwe P Diddy ankamenya chibwenzi chake ku hotel. Izi zingoonesa kuti zivuta ndithu.

Mulandu wu ukuyembekezeledwa kukhala miyezi yosapitilira iwiri, ndipo ma umboni alipo ambili osonyeza kuti P-Diddy ndi olakwa, koma pokuti ma lawyer awo anena kuti wawoyi ndi osalakwa tiye tikhale limodzi kuti tione kuti zenizeni ndi ziti.

Admin Jeffrey

Comment Below

upload your music with us to get maximum reach out!