Ndichifukwa chani ku Australia anthu amatha kuwalora kuvota atangovala Pant ekha?
Inde! Ku Australia ndi dziko lokhalo lomwe amatha kukulora kukavota utangovala pant ekha pazifukwa izi
Pamene mayiko ambili amavutika kulimbikitsa anthu kuti akalembetse komanso kuponya nawo vote, Ku Australia ndi dziko limodzi lomwe linaika lamulo lokhwima lokakamidza aliyense yemwe wakwana dzaka 18 kuti akavote.
Pa chifukwa chimenechi, anthu ena amatha kupita kovota atangovala kabudula wa mkati yekha (pant) pofuna kuonesa kuti akungoponya voti yo chifukwa ndi zokakamiza koma sakufuna kutelo pawokha.
Kwa onse amene atakane kuvota amalipilitsidwa ndalama yokwana $13 USD yomwe ku Malawi kuno MK23, 000. Okhawo amene ali ndi zifukwa zomveka bwino ndi amene amaloredwa kukhala osavota, zina mwa zitsanzo mwa zifukwazi monga kwa onse amene ali pa ulendo kapena ali kunja kwa dzikoli pa nthawi ya zisankhoyi.
Sizinathele pomwepa, akutiso kwa onse amene avota amalimbikisidwa kugula ndi kudya sausage ngati mbali imbodzi ya chikhalidwe pa nthawi ya zi sankho (democracy sausage).
Australia inali ndi zisankho zama Prime minister ndipo anthu okwana 18 Million ndi amene amayenela kuponya nawo vote pa 3rd May.
Zosatila zisankhozi wapambana ndi Anthony Albanese ndipo amene amapikisana nawo anthu sanawavotele chifukwa fundo zawo ambili zimawamvekela ngati za Trump, zomwe ambili sizinawagwire mtima
Source BBC